2 Chronicles 34:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chakuti anthuwo adandisiya Ine namapembedza milungu ina, nkumandichimwira ndi mafano ao, adaputa mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao, Ine pano mkwiyo wanga wayakira mzinda uno, ndipo sudzazima ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa iwo anasiya Ine ndi kufukiza lubani kwa milungu ina ndi kuwutsa mkwiyo wanga ndi zonse zimene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzatsanulidwa pamalo pano ndipo sudzazimitsidwa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, kuti autse mkwiyo wanga ndi nchito zonse za manja ao; cifukwa cace ukali wanga utsanulidwa pamalo pano wosazimika.