2 Chronicles 34:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti mtima wako walapa ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, utamva mau ake otsutsa mzinda uno ndi anthu onse am'menemo. Popeza kuti wadzichepetsa pamaso panga, nkung'amba zovala zako numalira pamaso panga, Inenso ndamva pemphero lako, ndatero Ine Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzichepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ake otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzichepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zovala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza mtima wako unali woolowa, ndipo wadzicepetsa pamaso pa Mulungu, pakumva mau ace otsutsana nao malo ano, ndi okhala m'mwemo, ndi kudzicepetsa pamaso panga, ndi kung'amba zobvala zako, ndi kulira pamaso panga; Inenso ndakumvera, ati Yehova.