2 Chronicles 34:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine ndidzakutenga, ukalondole makolo ako, ndipo udzaikidwa m'manda mwamtendere. Motero maso ako sadzaona zoipa zija zimene ndidzabweretsa pa mzinda uno ndi pa anthu ake.” Tsono anthu aja adabwerera nakanena mau amenewo kwa mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ndidzakusonkhanitsa kumakolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ine ndidzakutengera kwa makolo ako, ndipo udzayikidwa mʼmanda mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene Ine ndidzabweretsa pa malo ano ndi pa iwo amene amakhala pano.’ ” Choncho iwo anatenga yankho lakelo ndi kubwerera kwa mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ndidzakusonkhanitsa ku makolo ako, nudzaikidwa kumanda kwako mumtendere, ndi maso ako sadzapenya zoipa zonse ndidzafikitsira malo ano ndi okhala m'mwemo. Ndipo anambwezera mfumu mau.