2 Chronicles 34:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake, adakali mnyamata, adayambapo kumapembedza Mulungu wa Davide kholo lake. Ndipo pa chaka cha 12 adayamba kuchotsa akachisi opembedzerako mafano ku Yuda ndi mu Yerusalemu. Adachotsanso mafano, osema ndi osungunula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ulamuliro wake, iye akanalibe wamngʼono, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide abambo ake. Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri iye anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa malo azipembedzo, mafano a Asera, milungu yosema ndi mafano owumbidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lace; ndipo atakhala zaka khumi ndi cimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzicotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga,