2 Chronicles 34:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka mfumu idaimirira pamalo pake, ndipo idachita chipangano pamaso pa Chauta kuti idzatsata njira za Chauta, ndipo kuti idzasunga mau, malamulo ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndipo kuti idzagwiritsa ntchito mau a chipangano olembedwa m'bukulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inaimirira pokhala pake, nichita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda chotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ake, ndi mboni zake, ndi malemba ake, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, kuchita mau a chipangano olembedwa m'bukumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayimirira pa chipilala chake ndipo inachitanso pangano pamaso pa Yehova: kutsatira Yehova, ndi kusunga malamulo ake, machitidwe ake ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndi kumvera mawu a pangano olembedwa mʼbukulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inaimirira pokhala pace, nicita pangano pamaso pa Yehova, kuti adzayenda cotsata Yehova, ndi kusunga malamulo ace, ndi mboni zace, ndi malemba ace, ndi mtima wace wonse, ndi moyo wace wonse, kucita mau a cipangano olembedwa m'bukumu.