2 Chronicles 34:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu adagumula maguwa a Abaala, iyeyo ali pomwepo. Adagwetsa maguwa ofukizirapo lubani, ndiponso mafano a dzuŵa amene ankakhala pamwamba pake, adaŵagwetsa pansi. Adaphwanya mafano, osema ndi osungunula. Tsono adaŵaperapera mpaka kuŵasandutsa fumbi, ndipo adawaza fumbilo pa manda a anthu amene ankapereka nsembe kwa mafano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pake; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maguwa ansembe a Baala anagwetsedwa iye atalamulira. Anadula zidutswazidutswa maguwa ofukizira lubani amene anali pamwamba pake, ndipo anaphwanya mafano a Asera, milungu ndi zifaniziro zake. Anaziperapera ndipo anaziwaza pamwamba pa manda a amene ankapereka nsembe kwa mafanowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anagumula maguwa a nsembe a Abaala pamaso pace; nawalikha mafano a dzuwa anakwezeka pamwamba pao; naphwanya zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga; nazipera, naziwaza pamanda pa iwo amene adaziphera nsembe.