2 Chronicles 34:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adagwetsamo maguwa, naphwanyaphwanya mafano ndi zithunzi, mpaka kuzidyukula ngati fumbi. Ndipo adagwetsa maguwa ofukizirapo lubani m'dziko lonse la Israele. Pambuyo pake adabwerera ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israele, nabwerera kunka ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iye anagwetsa maguwa ansembe ndi mafano a Asera ndi kuphwanyaphwanya milungu yawo kukhala fumbi ndi kuduladula maguwa ofukizapo lubani mʼdziko lonse la Israeli. Atatero, anabwerera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nagumula maguwa a nsembe, naperapera zifanizo ndi mafano osema, nalikha mafano a dzuwa onse m'dziko lonse la Israyeli, nabwerera kumka ku Yerusalemu.