2 Chronicles 34:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha 18 cha ufumu wake, atayeretsa dzikolo pamodzi ndi Nyumba ya Chauta yomwe, Yosiya adatuma Safani, mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya, kazembe wa mzinda, kudzanso Yowa, mwana wa Yowahazi, mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Chauta Mulungu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma Safani mwana wa Azaliya, ndi Maaseiya kazembe wa mudzi, ndi Yowa mwana wa Yehowahazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya, atayeretsa dziko ndi Yerusalemu, Yosiya anatuma Safani mwana wa Azariya ndi Maaseya, wolamulira mzinda pamodzi ndi Yowa mwana wa Yowahazi mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Yehova Mulungu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atakhala mfumu tsono zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri, atayeretsa dziko ndi nyumbayi, anatuma safana mwana wa Azaliya, ndi Maseya kazembe wa mudzi, ndi Yona mwana wa Yoadazi wolemba mbiri, akonze nyumba ya Yehova Mulungu wace.