2 Chronicles 34:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa adadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama zimene adaabwera nazo ku Nyumba ya Chauta. Ndalamazo nzimene Alevi ndi alonda apakhomo adaasonkha ku dziko la Manase ndi la Efuremu ndi kwa anthu onse otsala a ku Israele, kwa onse a ku Yuda ndi a ku Benjamini ndiponso kwa nzika zonse za mu Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, napereka ndalama adabwera nazo kunyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira kudzanja la Manase ndi Efuremu, ndi kwa otsala onse a Israele, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anapita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe ndipo anamupatsa ndalama zimene zinaperekedwa mʼNyumba ya Mulungu, zimene Alevi amene anali alonda apakhomo analandira kuchokera kwa anthu a ku Manase, Efereimu ndi onse otsala a ku Israeli ndiponso anthu onse ochokera ku Yuda ndi Benjamini ndi okhala mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza kwa Hilikiya wansembe wamkulu, napereka ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Mulungu, zimene Alevi osunga pakhomo adasonkhanitsa kuzilandira ku dzanja la Manase ndi Efraimu, ndi kwa otsala onse a Israyeli, ndi kwa Yuda yense, ndi Benjamini, ndi kwa okhala m'Yerusalemu.