2 Chronicles 35:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapatula nsembe zopsereza, kuti azipereke potsata magulu a mabanja a anthu wamba, pamene ankapereka zao kwa Chauta, monga momwe zidaalembedwera m'buku la Mose. Ndipo adachitanso chimodzimodzi ndi ng'ombe zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anayika padera nsembe zopsereza kuti azipereke kwa magulu angʼonoangʼono a mabanja a anthu kuti apereke kwa Yehova monga zinalembedwa mʼbuku la Mose. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi ngʼombe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacotsapo nsembe zopsereza, kuti azipereke kwa ana a anthu monga mwa magawidwe a nyumba za makolo; azipereke kwa Yehova monga mulembedwa m'buku la Mose. Natero momwemo ndi ng'ombezo.