2 Chronicles 35:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adaotcha mwanawankhosa wa Paska pa moto, potsata mwambo. Adaphika nyama yamwanawankhosa ya Paska m'mbiya, m'mitsuko ndi m'ziwaya. Ndipo adazipereka mofulumira kwa anthu osakhala ansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaotcha Paska pamoto, monga mwa chiweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anawotcha nyama za Paska monga momwe zinalembedwera ndi kuwiritsa zopereka zopatulika mʼmiphika, mʼmitsuko ndi mʼziwaya ndipo anazipereka mofulumira kwa anthu onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaoca Paskha pamoto, monga mwa ciweruzo; koma zopatulikazo anaziphika m'miphika, ndi m'mitsuko, ndi m'ziwaya; nazipereka msanga kwa ana onse a anthu.