2 Chronicles 35:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ankakonza zao ndi za ansembe, chifukwa chakuti ansembe, ana a Aaroni, anali otanganidwa ndi kupereka nsembe zopsereza ndi kutentha mafuta mpaka usiku. Choncho Alevi ankakonza zao ndiponso za ansembe, ana a Aaroni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pambuyo pake anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; chifukwa chake Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Izi zitatha, anakonza zawo ndi za ansembe chifukwa ansembe, zidzukulu za Aaroni, anali otanganidwa kupereka nsembe zopsereza ndi mafuta a nyama mpaka madzulo. Choncho Alevi amakonza zawo ndi za ansembe, ana a Aaroni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pambuyo pace anadzikonzera okha ndi ansembe; popeza ansembe, ana a Aroni, analikupereka nsembe zopsereza ndi mafuta mpaka usiku; cifukwa cace Alevi anadzikonzera okha ndi ansembe ana a Aroni.