2 Chronicles 35:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu oimba nyimbo, ana a Asafu, anali atakhala m'malo mwao potsata lamulo la Davide, la Asafu, la Hemani ndi la Yedutuni, mneneri wa mfumu. Alonda apazipata anali ku chipata chilichonse. Choncho kunali kosafunika kuti achokepo pa ntchito yao, poti abale ao Alevi ankaŵakonzera zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi oimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu oyimba nyimbo, zidzukulu za Asafu, anali pa malo awo potsata zomwe analemba Davide, Asafu, Hemani ndi Yedutuni mlosi wa mfumu. Alonda apazipata anali pa chipata chilichonse ndipo kunali kosafunika kuti achoke pa ntchito yawo, poti abale awo Alevi ankawakonzera zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi oyimbira, ana a Asafu, anali pokhala pao, monga adalamulira Davide, ndi Asafu, ndi Hemani, ndi Yedutuni mlauli wa mfumu; ndi olindirira anali pa zipata zonse, analibe kuleka utumiki wao; pakuti abale ao Alevi anawakonzera