2 Chronicles 35:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ntchito zonse za Chauta zidakonzeka tsiku limenelo, kuti anthu achite Paska ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la Chauta, potsata lamulo la mfumu Yosiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kuchita Paska, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero pa nthawi imeneyi ntchito yonse ya Yehova ya chikondwerero cha Paska ndi nsembe zopsereza pa guwa la Yehova inachitika monga analamulira mfumu Yosiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo kutumikira konse kwa Yehova kunakonzeka tsiku lomwelo, kucita Paskha, ndi kupereka nsembe zopsereza pa guwa la nsembe la Yehova, monga analamulira mfumu Yosiya.