2 Chronicles 35:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sidachitikepo Paska yofanafana ndi imeneyi ku Israele chiyambire nthaŵi ya Samuele, mneneri uja. Panalibe ndi imodzi yomwe mwa mafumu a Aisraele imene idachitapo Paska monga imene adachita Yosiya, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, Ayuda ndi Aisraele onse amene analipo, kudzanso nzika za mu Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Panalibe Paska wochitika m'Israele wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samuele mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israele anachita Paska wotere, ngati ameneyu anachita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisraele opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paska yofanana ndi iyi sinachitikepo ku Israeli kuyambira nthawi ya Samueli ndipo palibe mmodzi mwa mafumu a Israeli anachitapo chikondwerero cha Paska ngati anachitira Yosiya pamodzi ndi ansembe, Alevi ndi Ayuda onse ndi Aisraeli amene anali pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Panalibe Paskha wocitika m'Israyeli wonga ameneyu, kuyambira masiku a Samueli mneneri; panalibenso wina wa mafumu a Israyeli anacita Paskha wotere, ngati ameneyu anacita Yosiya, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi Ayuda onse, ndi Aisrayeli opezekako, ndi okhala m'Yerusalemu.