2 Chronicles 35:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitapita zimenezi ndipo Yosiya atakonza Nyumba ya Chauta, Neko, mfumu ya ku Ejipito, adapita kukamenya nkhondo ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya adapita kukamenyana naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chitatha ichi chonse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aejipito anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Yufurate; ndipo Yosiya anamtulukira kuyambana naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi zitachitika, pamene Yosiya anakonzanso Nyumba ya Mulungu, Neko mfumu ya Igupto inapita kukachita nkhondo ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Citatha ici conse, Yosiya atakonza nyumbayi, Neko mfumu ya Aigupto anakwera kuyambana ku Karikemisi ku Firate; ndipo Yosiya anamturukira kuyambana naye.