2 Chronicles 35:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Neko adatuma amithenga kwa iyeyo kukamufunsa kuti, “Kodi iwe mfumu ya ku Yuda, ukuti tichitane chiyani? Ine sindibwera kudzalimbana ndi iwe lero, koma ndidzalimbana ndi banja limene ndikumenyana nalo nkhondo. Ndipo Mulungu wandilamula kuti ndifulumire. Siya kukangana ndi Mulungu amene ali nane, kuwopa kuti angakuwononge.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndili ndi chiyani ndi inu, mfumu ya Yuda? Sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndili nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kuvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Neko anatumiza amithenga kwa iye kunena kuti, “Kodi pali mkangano wanji pakati pa iwe ndi ine, iwe mfumu ya Yuda? Ine sindikuthira nkhondo iwe pa nthawi ino, koma nyumba imene ndili nayo pa nkhondo. Mulungu wandiwuza kuti ndifulumize choncho leka kutsutsana ndi Mulungu amene ali ndi ine, mwina adzakuwononga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Neko anatuma mithenga kwa iye, ndi kuti, Ndiri ndi ciani ndi inu, mfumu ya Yuda? sindinafika kuyambana ndi inu lero, koma ndi nyumba imene ndiri nayo nkhondo; ndipo Mulungu anati ndifulumire; lekani kubvutana ndi Mulungu amene ali nane, Iye angakuonongeni.