2 Chronicles 35:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yosiya sadachoke ndipo adadzizimbaitsa kuti amenyane naye nkhondo. Sadasamale mau a Nekoyo amene Mulungu adaalankhula, koma adakamenyana ku chigwa cha Megido.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yosiya sanatembenuke nkhope yake kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ochokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'chigwa cha Megido.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Yosiya sanatembenuke kumusiya iyeyo, koma anadzizimbayitsa ndi kukalowa mʼnkhondo. Iye sanamvere zimene Neko ananena molamulidwa ndi Mulungu koma anapita kukamenyana naye ku chigwa ku Megido.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yosiya sanatembenuka nkhope yace kumleka, koma anadzizimbaitsa kuti ayambane naye, osamvera mau a Neko ocokera m'kamwa mwa Mulungu; nadza kuyambana naye m'cigwa ca Megido.