2 Chronicles 35:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya nayenso adapeka nyimbo yamaliro chifukwa cha Yosiyayo. Anthu onse oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, akhala akunena za Yosiya pomlira mpaka lero lino. Zimenezi zakhala ngati mwambo ku Israele, ndipo zidalembedwa m'buku lotchedwa “Madandaulo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israele; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya anapeka nyimbo za maliro chifukwa cha Yosiya, ndipo mpaka lero lino amuna ndi akazi onse oyimba amakumbukira Yosiya pa nyimbo zawo za maliro. Izi zinakhala mwambo mu Israeli ndipo zinalembedwa mʼNyimbo za Maliro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yeremiya anamlembera Yosiya nyimbo yomlira; ndi oyimbira onse, amuna ndi akazi, amanena za Yosiya nyimbo za maliro zao mpaka lero lino; naziika zikhale lemba m'Israyeli; taonani, zilembedwa m'Nyimbo za Maliro.