2 Chronicles 35:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adauza Alevi onse amene ankaphunzitsa Aisraele ndipo anali opatulikira Chauta, kuti, “Muike bokosi lopatulika m'Nyumba imene Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israele, adamanga. Simuzidzalisenzanso pa mapewa anu ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisraele onse, ndiwo opatulikira Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ake Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati kwa Alevi amene amalangiza Aisraeli onse omwe anadzipatula kwa Yehova: Ikani bokosi lopatulika mʼNyumba ya Mulungu amene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli anamanga. Lisamanyamulidwe pa mapewa anu. Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati kwa Alevi akuphunzitsa Aisrayeli onse, ndiwo opatulima Yehova, Ikani likasa lopatulika m'nyumba imene Solomo mwana wa Davide mfumu ya Israyeli anaimanga; silikhalanso katundu pa mapewa anu; tsopano mutumikire Yehova Mulungu wanu, ndi anthu ace Israyeli.