2 Chronicles 35:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono muphe mwanawankhosa wa Paska, ndipo mudziyeretse. Muthandize abale anu, kuti zipherezere zimene Chauta adalankhula kudzera mwa Mose.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muphere Paska, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kuchita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muzipha ana ankhosa a Paska, muzidzipatula nokha ndi kuwakonzera abale anu ana ankhosa awo, kuchita zimene Yehova analamulira mwa Mose.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muphere Paskha, nimudzipatule ndi kukonzera abale anu, kucita monga mwa mau a Yehova ndi dzanja la Mose.