2 Chronicles 35:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nduna zakenso zidapereka mwaufulu kwa anthu, kwa ansembe ndi kwa Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a ku Nyumba ya Mulungu, adapereka kwa ansembe zopereka izi za Paska: anaankhosa ndi anaambuzi 2,600, ndiponso ng'ombe zamphongo 300.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi akulu ake anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehiyele, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paska.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi akulu ace anapatsa nsembe yaufulu kwa anthu, kwa ansembe, ndi kwa Alevi. Hilikiya ndi Zekariya ndi Yehieli, atsogoleri a m'nyumba ya Mulungu, anapatsa ansembe zoweta zazing'ono zikwi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi, ndi ng'ombe mazana atatu, zikhale nsembe za Paskha.

Recommended Reading