2 Chronicles 36:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomatha chaka, mfumu Nebukadinezara adatuma anthu kukamtenga, ndipo adabwera naye ku Babiloni, pamodzi ndi ziŵiya zamtengowapatali za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adakhazika Zedekiya mbale wake kuti akhale mfumu ya ku Yuda ndi Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babiloni, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi ya mphukira, mfumu Nebukadinezara inayitanitsa Yehoyakini ndipo inapita naye ku Babuloni, pamodzi ndi ziwiya zamtengowapatali za mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova, ndipo anayika Zedekiya malume wake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pofikanso nyengo, mfumu Nebukadinezara anatumiza anthu abwere naye ku Babulo, pamodzi ndi zipangizo zokoma za nyumba ya Yehova; nalonga Zedekiya mbale wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.