2 Chronicles 36:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapandukiranso mfumu Nebukadinezara amene anali atamlumbiritsa kwa Mulungu kuti adzamumvera. Koma Zedekiyayo adangoti nkhongo gwa, nkuumitsanso mtima wake, kuti asabwerere kwa Chauta, Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lake, nalimbitsa mtima wake kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawukiranso mfumu Nebukadinezara amene anamulumbiritsa mʼdzina la Mulungu. Iyeyo anali wosamva ndipo anawumitsa mtima wake. Sanatembenukire kwa Yehova Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso anapandukana naye mfumu Nebukadinezara, amene adamlumbiritsa pa Mulungu; koma anaumitsa khosi lace, nalimbitsa mtima wace kusatembenukira kwa Yehova Mulungu wa Israyeli,