2 Chronicles 36:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri onse a ansembe, pamodzi ndi anthu omwe, adachita zosakhulupirika zambirimbiri potsata zoipa za mitundu ina ya anthu. Adaipitsa Nyumba ya Chauta imene Chautayo anali ataipatula kuti ikhale yake ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso ansembe aakulu onse ndi anthu anachulukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene anapatula m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera apo, atsogoleri onse a ansembe ndi anthu ena anapitirapitira kukhala osakhulupirika, kutsatira machitidwe onse onyansa a mitundu ina ndi kudetsa Nyumba ya Yehova Mulungu wawo, imene anayipatula mu Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso ansembe akulu onse ndi anthu anacurukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene ana patula m'Yerusalemu.