2 Chronicles 36:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, Mulungu wa makolo ao, ankaŵatumira amithenga kaŵirikaŵiri, chifukwa chakuti ankaŵamvera chifundo anthu ake ndi malo ake amene Iye ankakhala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo ndi dzanja la mithenga yake, nalawirira mamawa kuituma, chifukwa anamvera chifundo anthu ake, ndi pokhala pake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova, Mulungu wa makolo awo, ankatumiza mawu kwa iwo kudzera kwa amithenga ake kawirikawiri, chifukwa ankawamvera chisoni anthu ake ndi malo ake okhalapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo, ndi dzanja la mithenga yace, nalawirira mamawa kuituma, cifukwa anamvera cifundo anthu ace, ndi pokhala pace;