2 Chronicles 36:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake adaŵautsira mfumu ya Ababiloni. Iwowo adapha anyamata ao ndi lupanga ku Nyumba ya Chauta wao. Ndipo sadachitire chifundo anyamata kapena anamwali, ndoda kapena nkhalamba. Chauta adaŵapereka onsewo kwa mfumu ya Ababiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anabweretsa mfumu ya anthu a ku Babuloni, imene inapha anyamata awo ndi lupanga ku malo opatulika, ndipo sanasiye kaya mnyamata kapena mtsikana, wamkulu kapena wokalamba. Mulungu anapereka onsewo kwa Nebukadinezara.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Akasidi, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osacitira cifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lace.