2 Chronicles 36:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaperekanso ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Chauta, zazikulu nzazing'ono zomwe, pamodzi ndi chuma chonse cha ku Nyumba ya Mulungu ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu, pamodzi ndi chuma cha nduna zake. Zonsezo adapita nazo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikulu ndi zazing'ono, ndi chuma cha nyumba ya Yehova, ndi chuma cha mfumu, ndi cha akalonga ake, anabwera nazo zonsezi ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ananyamula kupita nazo ku Babuloni zipangizo zonse za mʼNyumba ya Yehova Mulungu wawo, zazikulu ndi zazingʼono zomwe, ndi chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso chuma cha mfumu ndi akuluakulu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikuru ndi zazing'ono, ndi cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca mfumu, ndi ca akalonga ace, anabwera nazo zonsezi ku Babulo.