2 Chronicles 36:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene adapulumuka ku lupanga, adaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni. Kumeneko adasanduka anthu oitumikira mfumuyo ndi ana ake, mpaka ufumu wa Persiya utakhazikitsidwa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babiloni, nakhala iwo anyamata ake, ndi a ana ake, mpaka mfumu ya Persiya idachita ufumu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anagwira ukapolo anthu otsala amene anapulumuka ku lupanga ndi kupita nawo ku Babuloni, ndipo anakhala antchito ake ndi ana ake mpaka pamene ufumu wa Peresiya unakhazikitsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babulo, nakhala iwo anyamata ace, ndi a ana ace, mpaka mfumu ya Perisiya idacita ufumu;