2 Chronicles 36:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chaka choyamba cha ufumu wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adautsa mtima wa Kirusiyo, kuti alengeze ku maiko onse a ufumu wake mpaka kulemba kumene. Adachita choncho kuti zimene Chauta adaalankhula kudzera mwa Yeremiya zipherezere. Adati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau m'ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Peresiya, pofuna kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anakhudza mtima wa mfumu ya Peresiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse ndipo anazilemba:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Caka coyamba tsono ca Koresi mfumu ya Perisiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Koresi mfumu ya Perisiya, kuti abukitse mau m'ufumu wace wonse, nawalembenso, ndi kuti,