2 Chronicles 36:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu wakumwamba, wandipatsa ine maufumu onse pa dziko lapansi. Ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku Yuda. Aliyense mwa inu nonse amene ali munthu wa Chauta, Chauta Mulungu wakeyo akhale naye. Ndipo apite.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Kirusi mfumu ya Persiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Yehova Mulungu wake akhale naye, akwereko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimene mfumu Koresi ya Peresiya ikunena ndi ichi: “Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa ine mafumu onse a dziko lapansi ndipo wandisankha kuti ndimumangire Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ku Yuda. Aliyense wa anthu ake pakati panu, Yehova Mulungu wake akhale naye, ndipo apite.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Koresi mfumu ya Perisiya, Yehova Mulungu Wam'mwamba anandipatsa maufumu onse a pa dziko lapansi, nandilangiza ndimmangire nyumba m'Yerusalemu, ndiwo ku Yuda. Ali yense mwa inu a anthu ace onse, Yehova Mulungu wace akhale naye, akwereko.