2 Chronicles 36:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu ya ku Ejipito idakhazika Eliyakimu, mbale wake wa Yehowahazi, kuti akhale mfumu yolamulira ku Yuda ndi ku Yerusalemu. Ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Yehoyakimu. Koma Yehowahazi uja Neko adamtenga kupita naye ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mfumu ya Aejipito anamlonga Eliyakimu mng'ono wake mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lake likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehowahazi mkulu wake, namuka naye ku Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu ya Igupto inakhazika Eliyakimu, mʼbale wake wa Yehowahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasintha dzina la Eliyakimu kukhala Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yowahazi mʼbale wake wa Eliyakimu ndi kupita naye ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mfumu ya Aigupto anamlonga Eliyakimu mng'ono wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lace likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehoahazi mkuru wace, namuka naye ku Aigupto.