2 Chronicles 36:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nebukadinezara adatenganso ziŵiya za ku Nyumba ya Mulungu kunka nazo ku Babiloni. Ndipo adakaziika ku nyumba yake yaufumu ku Babiloniko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nebukadinezara anatenganso ndi zipangizo za nyumba ya Yehova kunka nazo ku Babiloni, naziika m'Kachisi wake ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nebukadinezara anatenganso zipangizo za ku Nyumba ya Yehova kupita nazo ku Babuloni ndipo anaziyika mʼnyumba ya Mulungu wake kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nebukadinezara anatenganso zipangizo za nyumba ya Yehova kumka nazo ku Babulo, naziika m'kacisi wace ku Babulo.