2 Chronicles 36:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ntchito zina zonse za Yehoyakimu ndi zoipa zimene ankachita zidalembedwa m'buku la mafumu a ku Israele ndi a ku Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Machitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zake anazichita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israele ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zochitika zina za pa ulamuliro wa Yehoyakimu, zinthu zonyansa zimene anachita ndi zonse zinapezeka kuti zinali zomutsutsa zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Macitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zace anazicita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.