2 Chronicles 4:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adapangitsanso zinthu zonse zimene zinali m'Nyumba ya Mulungu: ndiye kuti guwa lagolide, matebulo a buledi woperekedwa kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Solomoni anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolide lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Mulungu: guwa lansembe lagolide; matebulo pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Solomo anapanganso zipangizo zonse zinali m'nyumba ya Mulungu, guwa la nsembe lagolidi lomwe, ndi magome oikapo mkate woonekera;

Recommended Reading