2 Chronicles 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapanga thanki. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu, ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wake mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizunguniza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anayenganso thawale losungunula la mikono khumi kukamwa, lozunguniza, ndi msinkhu wace mikono isanu; ndi cingweca mikono makumi atatu cinalizunguniza.