2 Chronicles 4:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'munsi mwa milomomu adaazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pansi pake panali mafaniziro a ng'ombe zakulizinga, khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pake. Ng'ombe zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo zithunzi zangʼombe zazimuna mozungulira, zithunzi khumi pa theka la mita. Ngʼombezo zimajambulidwa mʼmizere iwiri ndipo anazipangira kumodzi ndi mbiyayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pansi pace panali mafanziro a ng'ombe zakulizinga khumi ku mkono umodzi, zakuzinga thawalelo pozungulira pace. Ng'ombezo zinali m'mizere iwiri, zinayengeka poyengedwa thawalelo.