2 Chronicles 4:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Thankilo kuchindikira kwake kunali ngati chikhatho. M'milomo mwake munkaoneka ngati m'milomo mwa chikho, ngati duŵa la kakombo. Munkaloŵa madzi okwanira malitara 60,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi kuchindikira kwake kunanga chikhato, ndi mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi zitatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbiyayo inali yochindikala ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 60,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi kucindikira kwace kunanga cikhato, ndi mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati luwa la kakombo; analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi zitatu.