2 Chronicles 4:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso mabeseni khumi osambiramo. Kumwera adaikako asanu ndipo kumpoto adaikakonso asanu. M'menemo ndimonso ankatsukiramo zinthu zimene ankagwiritsa ntchito popereka nsembe zopsereza. Koma m'thanki lalikulu lija ndimo m'mene ankasambiramo ansembe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anapanganso mbiya zaphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anapanga mabeseni khumi otsukira zinthu ndipo asanu amawayika mbali ya kummwera, asanu mbali ya kumpoto. Mʼmenemo amatsukiramo zinthu zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nsembe zopsereza koma mbiyamo ndi mʼmene ankasambiramo ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anapanganso mbiya zamphwamphwa khumi, naika zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere, kutsukiramo; za nsembe yopsereza anazitsuka m'menemo; koma thawale ndi la ansembe kusambiramo.