2 Chronicles 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Mulungu. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, ndipo adaika siliva, golide ndi ziŵiya zonse m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo zidatha ntchito zonse Solomoni adazichitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni anabwera nazo zopatulika zija za atate wake Davide; naziika siliva, ndi golide, ndi zipangizo zonse m'chuma cha nyumba ya Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ntchito yonse imene Solomoni anagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka; siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo zidatha nchito zonse Solomo adazicitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo anabwera nazo zopatulika zija za atate wace Davide; naziika siliva, ndi golidi, ndi zipangizo zonse m'cuma ca nyumba ya Mulungu. Kuperekedwa kwa Kacisi.