2 Chronicles 5:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anachita chipangano ndi ana a Israele potuluka iwo m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munalibe kanthu kena m'likasa, koma magome awiri Mose anawaika m'mwemo ku Horebu, muja Yehova anacita cipangano ndi ana a Israyeli poturuka iwo m'Aigupto.