2 Chronicles 5:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Alevi onse amene ankaimba nyimbo, Asafu, Hemani ndi Yedutuni, ana ao pamodzi ndi abale ao, ovala nsalu za bafuta wambee, ali ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe, adaimirira cha kuvuma kwa guwa, pamodzi ndi ansembe okwanira 120 amene ankaimba malipenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alevi omwe akuimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao ovala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi onse amene anali oyimba: Asafu, Hemani, Yedutuni ndi ana ndiponso abale awo, amayima mbali ya kummawa kwa guwa lansembe atavala zovala zofewa zosalala akuyimba ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe. Ansembe onse amene amayimba malipenga analipo 120 pamodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alevi omwe akuyimba, onsewo ndiwo Asafu, Hemani, Yedutuni, ndi ana ao, ndi abale ao obvala bafuta, ali nazo nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, anaima kum'mawa kwa guwa la nsembe, ndi pamodzi nao ansembe zana limodzi mphambu makumi awiri akuomba malipenga.