2 Chronicles 5:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ansembe adafika nalo Bokosi lachipangano la Chauta lija ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe analowa nalo likasa la chipangano la Yehova kumalo kwake m'chipinda chamkati mwa Kachisi, m'malo opatulika kwambiri, pansi pa mapiko a akerubi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a Akerubi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe analowa nalo likasa la cipangano la Yehova kumalo kwace m'moneneramo mwa kacisi, m'malo opatulikitsa, pansi pa mapiko a akerubi.