2 Chronicles 5:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mphikozo zinali zazitali kwambiri, kotero kuti nsonga zake zinkaonekera kukhalira ku malo opatulika kopambana patsogolo pa malo opatulika am'kati mwenimweni. Koma kunja sizinkaonekera. Ndipo zili komweko mpaka pano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa chakuno cha chipinda chamkati, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo zili komweko mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika, koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zinatalikitsa mphikozo, kuti nsonga za mphiko zidaoneka kulikasa cakuno ca moneneramo, koma sizinaoneka kubwalo; ndipo ziri komweko mpaka lero lino.