2 Chronicles 6:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri nkanthu, m'mimba mwake mamita aŵiri nkanthu, msinkhu wake mita limodzi ndi theka, ndipo anali ataimanga m'kati mwenimweni mwa bwalo. Adakwera pansanjapo, ndipo adagwada pa maondo ake, msonkhano wonse wa Aisraele ukuwona, iye anakweza manja ake kumwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni adapanga chiunda chamkuwa, m'litali mwake mikono isanu, ndi msinkhu wake mikono itatu, nachiika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo nagwada pa maondo ake pamaso pa khamu lonse la Israele, natambasulira manja ake kumwamba;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo anali atapanga nsanja yamkuwa, kutalika kwake kunali mamita awiri, mulifupi mwake munali mamita awiri, msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka ndipo nsanjayo anayimika pakati pa bwalo lakunja. Iye anayimirira pa nsanjapo nagwada pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo adapanga ciunda camkuwa, m'litali mwace mikono isanu, ndi kupingasa kwace mikono isanu, ndi msinkhu wace mikono itatu, naciika pakati pa bwalo; ndipo anaima pamenepo, nagwada pa maondo ace pamaso pa khamu lonse la Israyeli, natambasulira manja ace kumwamba;