2 Chronicles 6:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adati, “Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, palibe Mulungu wina wonga inu kumwamba kapena pa dziko lapansi. Mumasunga chipangano ndi kuwonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wao wonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Yehova Mulungu wa Israele, palibe Mulungu ngati Inu, m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira chipangano ndi chifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pa dziko. Inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Yehova. Mulungu wa Israyeli, palibe Mulungu ngati Inu, m'mwamba, kapena pa dziko lapansi, wakusungira cipangano ndi cifundo akapolo anu akuyenda pamaso panu ndi mtima wao wonse;