2 Chronicles 6:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza bambo wanga, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israele; malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao ndi kumayenda motsata malamulo anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wachifumu wa Israele; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'chilamulo changa, monga umo unayendera iwe pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo ndi kusunga malamulo anga monga iwe wachitira.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wakukhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; pokhapo ngati ana ako asamalira njira yao, kuti ayende m'cilamulo canga, monga umo unayendera iwe pamaso panga.