2 Chronicles 6:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Inu mumve kumwambako, ndipo muchitepo kanthu ndi kuŵaweruza atumiki anuwo. Wochimwa mugamule kuti ngwolakwa ndipo mumlange chifukwa cha zolakwa zakezo. Koma wosachimwayo mugamule kuti ngwopanda mlandu, ndipo mumpatse mphotho molingana ndi makhalidwe akewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mumvere m'Mwamba, nimuchite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa chilungamo chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
imvani kumwambako ndi kuchitapo kanthu. Weruzani atumiki anuwo, wochimwa mugamule kuti ndi wolakwa ndipo alangidwe chifukwa cha zimene wachita. Wosachimwa mugamule kuti wosalakwa, ndipo muonetse kusalakwa kwakeko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mumvere m'Mwamba, nimucite ndi kuweruzira akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera chimo lace, ndi kulungamitsa wolungamayo, kumbwezera monga mwa cilungamo cace.