2 Chronicles 6:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkutembenuka ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu okhala m'Nyumba muno,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anu Israele akawakantha mdani chifukwa cha kukuchimwirani, nakabwerera iwowa ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m'nyumba yino;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera pamaso panu mʼNyumba ino,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anu Israyeli akawakantha mdani cifukwa ca kukucimwirani, nakabwerera iwowa ndi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedzera pamaso panu m'nyumba yino;