2 Chronicles 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Inuyo mumve kumwambako, ndipo mukhululukire tchimo la anthu anu Aisraele. Kenaka muŵabwezenso ku dziko limene Inu mudaŵapatsa iwowo ndi makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire tchimo la anthu anu Israele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa iwo ndi makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mumvere Inu m'Mwamba, nimukhululukire chimo la anthu anu Israyeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.